CHANGALUME BARRACKS ILIPIRA K300,000
Bungwe la Football Association of Malawi lapereka chilango kwa timu ya Changalume Barracks kuti ilipire ndalama zokwana K300,000 kamba kolowera malo osayenerera mu bwalo.
Masabata awiri apitawo, timuyi inali ndi masewero ndi FOMO ku bwalo la Mulanje Park ndipo anagwiritsa ntchito kukwera pa chipata cholowera angakhale kuti galimoto yawo inadutsa pa chipata chenicheni.
Mu masewerowa, matimu awiriwa analepherana 0-0 ndipo mwa kuganiza, iyi inali njira ya zikhulupiliro.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores