NKHANI
Mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi Brigadier Gilbert Mittawa walengeza kuti sadzayima nawo pa zisankho za bungweli komanso zaku Football Association of Malawi chaka cha mawa.
Mittawa wati wachita izi ngati mbali ya utsogoleri kuti ukachita zabwino umasiyira ena kuti achiteko ndipo adzatula pansi mu April chaka cha mawa.
Iye wati ndi zodandaulitsa kuti ku mpira wa miyendo kwalowa ndale zochuluka kuleka kukweza masewero zomwe waona kuti sizili bwino.
Komabe Mittawa wati akukhulupilira kuti wasintha zinthu zambiri pomwe ligi yaikulu ikuyenda mwa ukadaulo ndipo ndi khumbo lake kuti wodzabwerawo asadzaphwasule ntchitoyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores