"TAKONZA MAVUTO ONSE NDIPO TIPAMBANA" - MUNTHALI
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake inali ndi nthawi yabwino yokonza mavuto omwe akhala akukumana nawo mu ligi ndipo ndi wokonzeka kuyamba kuchita bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akukumana ndi Ekhaya FC mu ndime ya matimu asanu ndi atatu amu chikho cha Airtel Top 8 loweruka pa bwalo la Bingu.
Iye wati mphunzitsi watsopano watimuyi, Wedson Nyirenda, wakhalanso akukonza zinthu zingapo pa nthawi yomwe wafika kutimuyi ndipo zonse tsopano zilibwino.
"Kuyang'ana ndi mmene tachitira zokonzekera zathu ndili ndi chikhulupiliro kuti tichita bwino ndithu chifukwa mavuto athu onse takonza," anatero Munthali.
Timuyi ndi yomwe ikuteteza chikhochi kamba koti achitenga kawiri kotsogozana ndipo inapeza malo mu chikhochi itamaliza pa nambala yachiwiri mu ligi ya chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores