"SIKUTI EKHAYA IZINGOGONJA NDI MATIMU AKULUAKULU" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati nthawi ikwana kuti timu yake izidzagonjetsa matimu akuluakulu mdziko muno komabe sikuti azingogonja akamakumana ndi matimuwa panopa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe akumane ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ya matimu asanu ndi atatu amu chikho cha Airtel Top 8 loweruka pa bwalo la Bingu.
Iye wati zitengera kakonzekeredwe ka timu yawo patsogolo pa masewerowa kuti akachite bwino koma chilimbikitso ndi chochuluka pa masewerowa.
"Tikungoyenera kuti tipite ndi mtima wolimbikira ndekuti tikachita bwino angakhale kuti Bullets ndi timu yaikulu komanso yasewerako kwambiri masewero ngati amenewa koma tikayesetsabe kuti tikachite bwino," anatero Chatama.
Iye watinso kubwerera kwake kutimuyi kuchokera ku tchuthi chomwe anapita ndi kwabwino ndipo akadayang'ana momwe omwe analipo amagwirira ntchito kuti ayambire pamenepo.
Awa akhala masewero oyamba kuti Ekhaya isewereko pa bwalo la Bingu komanso koyamba mu mpikisanowu omwe anapeza malo atathera pa nambala yachisanu ndi chiwiri mu ligi ya chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores