EAGLES SIKUPWEKETSA CIVIL
Timu ya Blue Eagles yati siyipanga chibwana chilichonse chiyiphweketsa timu ya Civil Service United kamba koti sikuchita bwino ndipo apita ndi mtima wokapeza chipambano pa masewero omwe akukumana.
Mphunzitsi watimuyi, De Kleck Msakakuona ndi yemwe wanena za nkhaniyi patsogolo pa masewero awo pa bwalo la Bingu loweruka mu ndime ya matimu asanu ndi atatu mu chikho cha Airtel top 8.
Iye wati timu yake yakonzekera bwino mmasewerowa ndipo akufunitsitsa kuti akagwiritse ntchito mipata yomwe akayipeze mu masewerowa.
"Ifeyo sitikuyiphweketsa Civil chifukwa nayo ndi timu yabwino nde Ife tikupita ndi mtima wokalimbikira kuti ngati tingapeze mwayi tipeze zigoli zomwe titatipeputsire ntchito tikamadzapita mmasewero achibwerenza," anatero Msakakuona.
Ndipo mtsogoleri wa wosewera kutimuyi, Gilbert Chirwa, wati bwalo la Bingu ndi la mwayi kutimu yawo.
"Ndasewera kwambiri Blue Eagles nde masewero omwe tasewera pa Bingu takhala tikuchita bwino nde nditha kunena kuti ndi
pakhomo pathu chifukwa zikho zonse zija tatengera pamenepa," anatero Chirwa.
Timu ya Blue Eagles inazigulira malo mu mpikisanowu itakwanitsa kumaliza pa nambala yachinayi mu ligi ya chaka chatha yomwe ankasewera akuchokera ku ligi yaing'ono.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores