"OYIMBIRA AMATUKWANA ZA MKABUDULA" - NDOLO
Mphunzitsi watimu ya Changalume Barracks, Davie Ndolo, wati ndi wokhumudwa ndi oyimbira pa masewero awo ndi Extreme kamba koti wathandizira kuti agonje komanso amatukwana osewera.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 pa bwalo la Owen Malijani ku Mchinji ndipo akukhulupilira kuti oyimbira watenga gawo lalikulu kuti agonje.
"Ziganizo zambiri zinali zokomera anzathuwo basi chomwe amafuna ndi kuti atibalalitse komanso anamutukwana kaputeni wathu za mkabudula nde zisamakhale chonchi chifukwa kumeneku ndiye kupha mpira," anafotokoza Ndolo.
Komabe iye wati ali ndi timu yabwino kwambiri yomwe ikungofunikira kukonza mavuto omwe akumana nawo kenako ayamba kuchita bwino.
Tsopano timuyi yagonja mu masewero awo awiri onse mu ligi ndipo ali pansi penipeni opanda point iliyonse mu ligi ya NBS Bank National Division.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores