NKHANI
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets itumiza osewera awo a zaka zosadutsa 17 Ku mpikisano wa mdziko la Zambia womwe timu ya Kafue Celtic ukuchititsa.
Izi zadziwika ndi lipoti ya mtolankhani wodziwika bwino mu dzikolo, Kaumba Chikenge.
Ena mwa matimu omwe atenge nawo mbali mu mpikisanowu ndi monga Zambia U-17 Select, Ascent Soccer Academy ya ku Malawi komanso matimu ena aku DRC ndi Zimbabwe akhale akuyitanidwanso.
Timu ya Kafue Celtic ikuchititsa masewerowa ndi cholinga chifukwa kupeza osewera atsopano omwe ndi aluso koma ali achisodzera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores