Timu ya TS Galaxy yapereka mwayi ku timu ya Orlando Pirates kuti ipambane ligi ya Betway Premiership yaku South Africa kutsatira kugonjetsa Mamelodi Sundowns 3-2 lachiwiri.
Sundowns ili pa mtunda pa ligiyi koma yamaliza masewero awo ndipo ikutsogola ndi mapoints atatu pamwamba pa Pirates yomwe ili ndi zigoli zochuluka mu ligi.
Izi zikutanthauza kuti chipambano chimodzi ndi chokwanira Kuti Orlando Pirates itenge ligi ya mdziko la South Africa poti yatsala ndi masewero awiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores