MITENGO YA DERBY YATULUKA
Mitengo ya masewero a matimu a Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets mu ligi yaikulu ya mdziko muno yatuluka pomwe anthu akungofunikira K8,000 Kuti awonere masewero aakuluwa.
Malingana ndi mitengo yomwe yatulutsidwa, K8,000 ndi mtengo wa tikiti yoguliratu koma pakhomo azikagulitsa K10,000 kuja kokhala aliyense.
Ndipo malo a VIP komwe kumakhala anthu olemekezeka ndi achuma chawo akaguliratu tikiti apereka K20,000 koma tsiku la mpira ndi K25,000.
Kulinso malo omwe ndi tizipinda ndipo anthu okwana 10 amakhalako uku akuonera mpira kwinaku akudya ndi kumwerera, uku ndi K30,000 munthu mmodzi.
Anthu akhonza kugula matikiti pa Area 18 Puma, Kafoteka Filling Station, Maula Puma, Mbowe Puma, ku nyumba ya Wanderers ku Blantyre komanso galimoto zomwe zikhale zikuyendayenda mu Lilongwe ndi Blantyre.
Matimuwa akumana kale kamodzi Chaka chino mu chikho cha NBS Bank Charity Shield ndipo Manoma anagweba Maule 1-0 ndi chigoli cha Sama Thierry Tanjong.