"Zikufunika kuti alimbikire" - Fazili
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati ayesetsa kuthandizira katswiri womwetsa zigoli Deborah Henry kuti achite bwino ndikupeza malo mu timuyi kamba ka ukadaulo omwe ali nawo pomwetsa zigoli koma zitengera kuti mwini wake alimbikira motani.
Iye amayankhula pomwe amayitana mndandanda wa osewera omwe apite ku m'bindikiro kukonzekera mpikisano wa COSAFA ndipo wamutenga Henry pomwe anasiyidwa ulendo wapitawo.
Fazili wati kutengedwa kwa katswiriyu sikukutanthauza kuti apita nawo ku South Africa koma akuyenera kulimbikira.
"Ndi osewera wabwino ndipo ndi momwe amachinyira zigoli zikuonekeratu kuti ndi wabwino koma tsopano akuyenera kupikisana ndi anzake ndipo akachita bwino apita nawo ku South Africa," iye anatero.
Iye anatinso Madyina Ngulube naye akuyenera kuonetsa kuti atha kuchita bwino pakuti pakatipa pabweranso osewera abwino ambiri pa malo akewo.
Henry anamwetsa zigoli 23 mu masewero 18 a ligi ya National Bank ndipo ndi yemwe anamwetsa zigoli zochuluka kuposa aliyense.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores