Bullets yakana zochotsa osewera
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yakana zoti yachotsa osewera ake kutimuyi kutsutsa malipoti omwe akhala akuzungulira pa masamba a mchezo loweruka.
Timuyi yachita izi kamba ka kalata yomwe ena apanga yoonetsa kuti yachotsa osewera asanu ndi atatu kamba kosowa khalidwe, kusasewera bwino komanso kutha kwa mgwirizano wawo.
Koma Bullets yanenetsa kuti malipotiwa ndi abodza ndipo timu yawo sinachiteko chiganizo onga chimenechi.
Iwo auza masapota awo kuti azidikira zomwe zimalembedwa pa masamba awo ovomerezeka kuti azidziwa chenicheni chomwe timu ikupanga.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores