''Tikuyenera kukonzanso ndi kuonjezera osewera'' - Mponda
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Mponda, wati anthu omwe amafuna kuti timuyi izitenga chilichonse akuyenera kulingaliranso kuti kodi timuyi ili ndi osewera oyenera kuterowo poti akufunikira kukonzanso timuyi.
Iye amayankhula kutsatira kufanana mphamvu 0-0 ndi Mighty Tigers zomwe zapereka mwayi kwa Mighty Wanderers kuti apambane ligi ndipo Mponda wati timu yake ikuyenera kuonjezeranso osewera kuti ikhale bwino.
''Anthu amaganiza kuti Bullets itha kumatenga chilichonse koma akuyenera kuganiziranso kuti ili ndi osewera apa mulingo umenewowo. Tikuyenera kuonjezera osewera ndi kukonzanso zambiri pa osewerawa,'' anatero Mponda.
Iye koma wayamikira osewera ake kuti ngakhale panali mavuto, iwo anayinyamulabe timuyi mpaka kufika kumapeto.
Bullets ili pa nambala yachiwiri pomwe ili ndi mapoints 63 pa masewero 29 omwe asewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores