Bungwe la FAM lalembera kalata Hassan Kajoke ndi nthumwi yake Ken Mvula komanso matimu a FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers kuti lachiwiri pa 16 May, 2023 akayambe kumva za mlandu wa osewerayu.
Silver Strikers inasuma kuti Kajoke anadya ndalama zatimuyi komanso anasaina kontrakiti ndi timuyi zomwe zabwelesa mpungwepungwe chifukwa osewerayu akusewera ku Bullets pano.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores