Bungwe la Football Association of Malawi (FAM) lalengeza kuti kuyambira chaka chino matimu aang'ono (reserve teams) sadziloledwa kutenga nawo gawo mu zikho m'mene muli matimu akulu akulu.
Zolengezazi zadza kutengera mkumano wa FAM womwe unaliko loweluka lapitali ku Salima ndipo mkulu woyang'anira za mipikisano ku FAM, Gomezgani Zakazaka ndi amene watsimikiza izi.
Malamulo a club licensing samalora matimu aang'ono kutenga nawo gawo mu chikho chomwe muli matimu akuluakulu.
A Zakazaka aonjezera kunena kuti matimu aang'onowa azichotsedwa akafika mundime yapadziko lino. Matimu aang'onowa ndi ololedwa kufikira mundime yachipulula yokha basi.
Chaka chatha timu ya Bullets yaying'ono inakumana ndi Bullets yayikulu mundime yotsiriza ya chikho cha FDH Bank zomwe zinabweretsa zokamba zambiri kwa anthu otsatira mpira.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores