Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la Football Association of Malawi (FAM) likuyembekezeka kulemba ntchito mphunzitsi ongogwirizira wa timu ya Malawi kumathero a sabata lino.
Izi ndi malingana ndizomwe yalemba nyuzipepa ya Times lero.
FAM inalengeza kuti sionjezera mgwirizano wake ndi mphunzitsi wa ku Romania, Mario Marian Marinica yemwe mgwirizano wake ukutha kumathero kwa mwezi uno.
FAM ikuyembekezereka kukasankhanso anthu ena mu komiti yoona za kagwiridwe ntchito ka mphunzitsi kapena kuti Sub-technical committee omwe akalowe mmalo mwa Tiya Somba Banda ndi Sugzo Ngwira.
A Tiya Somba Banda anagonja pa masankho a Bungwe la Super League of Malawi, Sulom ndi Fleetwood Haiya.
Sugzo Ngwira wagonja pa masankho a National Women's Football Association pamaso pa Adelaide Migogo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores