Timu ya Salima Secondary School yamaliza pa nambala yachitatu mu mpikisano wa African Schools Championship pomwe yagonjetsa Sainte Rite ya ku Benin 3-1 ku Durban, South Africa.
Blessings Sakala, Ishmael Bwanali ndi Latumbikika Kayira ndi amene anamwetsa zigoli za Salima.
Timuyi ilandira mendulo ya bronze🥉 ndi ndalama $ 150, 000 (pafupifupi K150 million).
Isanasewere masewerowa Salima inagonja ndi Ben Sekou ya ku Guinea 2-0 mu ma Semifinal.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores