"ZIKUONEKA KUTI TIKAPEZA ZOTSATIRA ZABWINO" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Masters Football Club Peter Mponda wati osewera ake akuoneka bwino pa bwalo la zamasewero malingana ndi kakonzekeredwe kawo ndipo akukhulupilira kuti akachita bwino ku Blantyre.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe timuyi ikumane ndi FCB Nyasa Big Bullets ku bwalo la Mpira lolemba ndipo wati timu yake yakonzekera bwino mmasewerowa.
"Akhala masewero ovuta kwambiri koma ifeyo takonzekera bwino ndipo anyamata akuoneka kuti azitolera kuti pakutha pa masewerowa tikapeze zotsatira zabwino," anatero Mponda.
Iye watinso timuyi inagonja ndi Ekhaya pa bwalo lomwe akupitalo kamba koti osewera awo anazolowera kapinga womera osati wachizungu komabe sichidzakhala chonamizira pa masewerowa.
Iye watinso osewera onse alipo pomwe Philimon Ndhlovu wachira koma Rafick Namwera ndi yemwe sapezeka kwa masabata angapo.
Timuyi ilowa mu masewerowa ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi ndi mapointsi okwana 12 pa masewero as
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores