MITHI SAPEZEKA KWA MASABATA ANAYI
Timu ya Mighty Wanderers ikuyembekezeka kukhala opanda wosewera wawo Lameck Mithi yemwe kuvulala kwake akhale masewero anayi osasewera.
Mphunzitsi watimuyi Bob Mpinganjira watsimikiza za nkhaniyi pomwe amafotokoza momwe timuyi ilili patsogolo pa masewero awo ndi Goshen City Dedza Dynamos lamulungu.
Iye wati vuto la Mithi lafika ku chipatala tsopano komwe akhalebe masabata anayi osasewera koma Alex Kambirinya wabwerera pomwe wachira.
"Apanso Emmanuel Nyirenda wavulala ndipo madotolo akumuyeza kuti awone kuti ali motani ndekuti tikhala wopanda Mithi komanso Nyirenda," anatero Mpinganjira.
Mithi wakhala wosewera wofunikira kwambiri kumbali ya Mighty Wanderers kamba koti wagoletsa zigoli zisanu mj ligi yaikulu ndi chimodzi mu chikho kumbali ya Manoma.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores