"TAPANGA TIMU YABWINO KWAMBIRI" - MAKONYOLA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Audlow Makonyola, wati akukhulupilira kuti wasonkhanitsa timu ya osewera abwino yomwe yisiyane ndi zaka zammbuyozi ndipo akuyembekezera kuyamba mwapamwamba mu ligi.
Iye amayankhula pomwe akukumana ndi timu ya Masters FC pa bwalo la Karonga lamulungu ndipo wati sakuyidelera kamba koti yatenga osewera omwe ndi amkhala kale mu ligi yaikulu.
Komabe iye wati akukhulupilira kuti timu yake ikhala yapamwamba akaona osewera omwe yasonkhanitsa chaka chino.
"Ndikukhulupilira kuti tapanga timu yabwino kuposa azaka za mmbuyomu chifukwa ndatenga osewera ku timu yaing'ono koma aluso kwambiri," iye anafotokoza.
Iye watinso osewera omwe anali odalilika kwambiri koma anali ovulala tsopano achira ndipo apezeka mmasewerowa.
Karonga ikuyamba tsopano masewero awo mu ligi kutsatira kulephereka kwa masewero awo mu sabata yoyamba ndi Mighty Wanderers zomwe Makonyola wati wawadekhetsa osewera zitawasokoneza kale.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores