"TANGOTSALA PANG'ONO KUTI TIMU IWOPSE" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati timu yake yapeza osewera apamwamba omwe angotsalira pang'ono kuti ikhale timu yoopsa kwambiri mdziko muno.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Red Lions loweruka pa bwalo la Mpira ndipo wati iwo akonzeka bwino pa masewerowa.
Iye anati timu yake yangotsala kuti aziyankhulana komanso kusatayilira kenako timu yake ikhala yokwana bwino.
"Tapeza osewera abwino kwambiri omwe asewera limodzi pa masewero apaubale tisanayambe ligi nde zangotsala zochepa kwambiri kuti tipange timu yamphamvu," iye anatero.
Patsogolo pa masewerowa, iye anati osewera onse alipo kupatulako wotchinga pagolo wawo Joshua Waka yemwe sapezeka kamba kovulala.
Ekhaya inayamba ndi kugonja 2-1 ndi Blue Eagles mu sabata yoyamba ndipo ili pa nambala 14 mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores