Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wabwera kuchokera ku Ulaya komwe anali koonjezera nzeru za uphunzitsi mmayiko a Scotland ndi England.
Mpinganjira wafika mdziko muno kudzera pa bwalo la ndege la Bakili Muluzi ku Chileka mu mzinda wa Blantyre.
Iye wati waphunzira zinthu zochuluka kwambiri zomwe zithandizire timu yake mu ligi ya Chaka cha 2026-27.
"Ndaphunzirako kuti nkhani ya madyedwe ndi yofunikira kwa osewera athu kuti si chakudya chilichonse chimene osewera akuyenera kudya," anatero Mpinganjira.
Timu ya Wanderers yakhala ili pansi pa MacDonald Mtetemera yemwe watengetsako chikho cha NBS Bank Charity Shield masabata awiri apitawo.
Mtsogoleri wa timuyi, a Dr Thomson Mpinganjira analonjeza kutumiza mphunzitsiyu ku ulaya ndipo atumizanso Mtetemera ku South Africa ku maphunzironso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores