SULOM IPATSIDWA CHILANGO NDI FAM
Bungwe la Football Association of Malawi lalengeza kuti lipereka chilango Ku bungwe la Super League of Malawi kamba kokanika kumvera ziganizo za bungweli angakhale kuti ali pansi pawo.
Izi zadziwika lamulungu masana pomwe mtsogoleri wa FAM, Fleetwood Haiya anapangitsa msonkhano wa atolankhani pamodzi ndi komiti yaikulu ya bungweli yomwenso mtsogoleri wa SULOM, Brigadier Gilbert Mittawa analipo.
Haiya wati panalibe mpungwepungwe pakati pa mabungwewa kamba koti FAM inayesera kulangiza SULOM mwa chikondi powalembera makalata koma Iwo anakanika kumva.
Iye wapepesa kwa a Malawi, matimu a Mighty Wanderers ndi Karonga United, anduna a zamasewero komanso FDH Bank kamba za momwe zinakhalira loweruka koma wati analolera kuti lamulo ligwire ntchito.
Mwa izi, SULOM ikhala ikuyitanitsidwa ku FAM kuti akamve chifukwa chomwe anakanira kutsata ziganizozi ndipo chilango chibwera chomwe chitha kufika kothetsa bungweli.
"SULOM ndi mwana wa FAM yemwe anangopatsidwa m
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores