BREAKING NEWS
FDH Bank yaimitsa thandizo lililonse lomwe limayika Ku mpira kudikira kuti zonse ziunikidwe bwinobwino.
Bankiyi yati yakhumudwa ndi kukokanakokana kwa mabungwe a Football Association of Malawi ndi Super League of Malawi pa nkhani ya kupezeka kwa bwalo la Kamuzu pa mwambo wotsegulira ligi yaikulu ya FDH Premiership.
Ndipo bankiyi yaimitsa Kaye thandizo lawo Ku timu ya dziko lino ya Flames komanso ligi ya FDH Premiership kamba koti anyazitsidwa ndi mpungwepungwewu.
Iwo ati pakufunika kuunikidwa kwapadera pa momwe thandizo lawoli limapitira ndipo ngati zigwirane ndi zomwe amakhulupilira pa ntchito pawo adzapanganso chiganizo cha iwo okha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores