BREAKING
Bungwe la Football Association of Malawi latulutsa kalata yofotokoza kuti bwalo la Kamuzu likadali lotseka ndipo silikuyenera kuchititsa masewero a Mighty Wanderers ndi Karonga United.
Kalatayi yatuluka patangodutsa maola angapo pomwe Super League of Malawi inati yakambirana ndi FAM kuti masewerowo achitike kamba koti bwaloli ndi lalikulu kuchititsa mwambo wotsegulira ligi.
Koma FAM yanenetsa kuti ngati masewero angachitike, SULOM ilandira chilango malingana ndi malamulo a bungweli.
Ndipo mtsogoleri wa FAM, Fleetwood Haiya, ndiyemwenso wagawa nawo uthengawu kusonyeza kuti panalibe kukambirana kulikonse pakati pa SULOM ndi FAM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores