FAM YAPEPESA KWA MFUMU YAKU LILONGWE
Bungwe loyendetsa mpira mu dziko lino la Football Association of Malawi latulutsa kalata yopepesa kwa mfumu ya mzinda wa Lilongwe, a Peter Banda, kamba kokanizidwa kukapereka nawo mphoto kwa osewera pamathero a chikho cha NBS Bank Charity Shield.
Izi zadza patangodutsa maola ochepa unduna wa achinyamata, chikhalidwe ndi masewero komanso mtsogoleri wa bungwe la ma khonsolo mdziko muno, a Isaac Jomo Osman, anauza FAM kuti ipepese.
Bungweli lati silinachite kukonza kuti lichitire chipongwe mfumuyi koma ena omwe amayendetsa zinthu pa bwalo pomwepo anaona kuti zinthu zina zisokonekera malingana ndi momwe anakonzera.
Iwo ati akufufuza momwe zinthu zonse zinayendera kuti apeze chenicheni chimene chinachitika pa mwambowu.
0995587166
0991769328
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores