UNDUNA WA ZAMASEWERO WAUZA FAM KUTI IPEPESE
Unduna wa achinyamata, chikhalidwe ndi masewero wadzudzula zomwe zinachitika pa masewero amu chikho cha Charity Shield pomwe mfumu ya mzinda wa Lilongwe, a khansala Peter Banda, analetsedwa kukapereka nawo mphoto pakutha pa masewerowa.
Mu kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu, Jeremiah Ndalama, yati ndi yokhumudwa ndi mchitidwewu ndipo yapempha Football Association of Malawi ipepese kamba ka mchitidwewu.
Undunawu watinso FAM ilembe lipoti pa chifukwa chenicheni chomwe mfumuyi inakanizidwira kufika pa malo operekera mphotozi komanso kuti apereke chilango kwa onse okhudziwa.
A Banda analetsedwa kukapereka mphoto kwa matimu a Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets omwe anakumana pa masewerowa ati kamba koti anavala zovala zosiyana ndi ena omwe anakapereka mphotozi.
Timu ya Wanderers ndi yomwe inali akatswiri a chikhochi kutsatira kupambana 1-0 ndi chigoli cha Sama Thierry Tanjong.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores