"ATSOGOLERI AMALIMBIKITSA OSEWERA ENA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, timu yake ikusowekera zintchito za atsogoleri awo, Tabitha ndi Temwa Chawinga, kuti ikhale ya chikwanekwane kupita ku mpikisano wa Womens African Cup of Nations.
Iye amayankhula pomwe amaunikira mmene timuyi yachitira ku mpikisano wa FIFA Series womwe athera pamapeto mu dziko la Kenya atagonja ndi Australia ndi India.
Fazili akukhulupilira kuti Scorchers ikufunikira awiriwa kamba koti amapereka chilimbikitso kwa osewera ena omwe akusewera mdziko muno.
"Timu ndi yokwana mwina tikungosowekera atsogoleri atimuyi chifukwa akapezeka timu imachita bwino komanso amalimbikitsa osewera ena akamawaona akulimbikiranso," anatero Fazili.
Iye wati osewera a timuyi akangochotsa mtima wa mantha komanso kudelera matimu ena ziwathandize kuti azichita bwino.
Malawi ikuyembekezeka kusewera mpikisano wake woyamba wa chikho cha WAFCON mu mwezi wa July ku Morocco.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores