Ma bwalo a Kamuzu, Nankhaka ndi Mzuzu alephera mulingo
Bungwe la Football Association of Malawi lapeza mabwalo a Kamuzu, Nankhaka ndi Mzuzu kuti sanafikire mulingo wochititsa masewero akuluakulu a mdziko muno.
Bungweli linayendera mabwalo 21 patsogolo pa ligi ya chaka chino ndipo mabwalo atatuwa ndi omwe apezedwa kuti sali mu mulingo wabwino.
Mabwalo a Chitipa, Karonga, Rumphi, Chitowe, Champions, Dimba, Silver, Civo, Bingu, Dedza, Mulanje, Joyce Chitsulo, Zomba ndi Mpira ndi omwe avomerezedwa.
Ndipo mabwalo ena a Owen Malijani, Kasungu, Balaka ndi Mchinji avomerezedwa kuchititsa masewero amu ligi yachiwiri ya mdziko muno.
Mkulu woyang'ana za ntchitoyi, Clement Kafwafwa wati ena bwalo ndi oyang'anira anapatsidwa nthawi yakukonza mabwalowa atayendera koyamba mu January.
Iye wati bungweli lipitilira kuyenderabe mabwalo onse mdziko muno kuti awonetsetse kuti ali pa mulingo woyenera.