"NDINE WOKONDWA POTI OSEWERA KUTSOGOLO AKUGOLETSA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati ndi wokondwa kuti osewera omwe amasewera kutsogolo kwa timuyi akukwanitsa kumwetsa zigoli zomwe zikupereka chiyembekezo kutimuyi chaka chino.
Makawa amayankhula izi atatha masewero omwe anagonjetsa Goshen City Dedza Dynamos 3-0 kuti atenge chikho cha Easter Elite Central Region Football Bonanza lolemba pa bwalo la Dedza.
Iye wati mpikisanowu wakhala wofunikira poti waonetsa pomwe matimu akusowekera ndipo akukhulupilira kuti timu yake igwiritsa ntchito zomwe yapeza za mpikisanowu.
"Ndili wokondwa kuti osewera akutsogolo akukwanitsa kugoletsa zigoli zomwe zinali vuto lathu mu zaka zapitazi ndekuti chaka chino titha kukhala ndi mpikisano wabwino," iye anatero.
Mu mpikisanowu, Civil inagonjetsa Kamuzu Barracks 1-0 ndi chigoli cha Muhammad Biason isanagonjetse Blue Eagles 1-0 ndi chigoli cha Madalitso Maso yemwenso anagoletsa chigoli choyamba ndi Dedza, China Chirwa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores