BWALO LA MPIRA LAKHAZIKITSIDWA KU MALAWI
Bungwe la Football Association of Malawi lakhazikitsa bungwe lomwe liziweruza milandu yosiyanasiyana lotchedwa National Discipline Resolution Chamber.
Mtsogoleri wa bungweli, Fleetwood Haiya wati bungwe la FIFA linapereka mwayi kuti milandu yokwe imakonzedwa ku bungweli liziweruzidwa mmayiko momwemo.
A Haiya ati bungweli likhala loyima palokha ndipo FAM silowererapo pa kagwiridwe ntchito ka bwaloli.
Iwo ati malamulo a bwaloli ayikidwa poyera kuti anthu onse aku mpira adziwe tsatanetsatane wa malamulowa.
Bwaloli litsogoleledwa ndi a Justice Chikopa ndipo milandu yonse yokhudza mpira wamiyendo izikambidwa ku bwaloli.
Ngati anthu sazikhutira ndi chigamulo cha bwaloli, azitha kukamang'ala ku bwalo laku FIFA la Court of Arbitration.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores