Mlimbika, Mkandawire ndi Kenneth alimbirana mphoto ya osewera wachichepere wachitsikana
Bungwe la Football Association of Malawi latulutsa ndandanda wa osewera omwe apikisane pa mphoto ya osewera yemwe wachita bwino wachichepere koma wachitsikana mu chaka cha 2025-26.
FAM yatulutsa mayinawa pokonzekera mwambo wopereka mphoto kwa anthu osiyanasiyana omwe achita bwino mu masewero osiyanasiyana mdziko muno.
Katswiri wa Kukoma Ntopwa Queens, Sarah Mlimbika ndiye dzina loyamba. Iye anakwanitsa kupeza mphoto zisanu zoti wasewera bwino pa masewero zomwe waposedwa ndi Deborah Henry yekha mu ligi yomwe anagoletsa zigoli zitatu komanso kuthandizira zitatunso.
Iye wachitanso bwino ku timu ya osewera osadutsa zaka 20 komansotu wasewererako timu yaikulu ya dziko lino mu masewero osiyanasiyana kuphatikiza COSAFA.
Wina ndi Mayamiko Mkandawire wa Ascent Academy. Pa masewero 15 amu ligi, anagoletsa zigoli 15 ndi kuthandizira ziwiri kuti atenge mphoto zosewera bwino zinayi.
Iye wasewereranso timu ya Osewera osadutsa zaka 20 ndipo anamwetsako chigoli chimodzi pa masewero awiri.
Omaliza ndi Maureen Kenneth Ascent Academy. Iye anakwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri ndi kuthandizira zinayi kuti apate mphoto zinayi zoti wasewera bwino pa masewero. Pa masewero 18 onse omwe wasewera sanachinyitseko 10 ngati wotseka kumbuyo.
Iye wasewera masewero onse a timu ya dziko lino yosadutsa zaka 20 komanso kukhala mbali ya timu yaikulu ya dziko lino.
Wopambana akalandira mphoto ku mwambo womwe ukachitikire ku Comesa mu mzinda wa Blantyre pa 06 March 2026.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores