HAMMERS ILIPIRA K100,000
Bungwe la Football Association of Malawi lapereka chilango ku timu ya Mzuzu City Hammers kuti alipire K100,000 kamba kokanika kupereka pa mkumano omwe umachitika masewero asanachitike.
Bungweli lapeza timuyi yolakwa kamba koti dongosolo lililonse la masewero limakakambidwa pa mkumanowu zomwe Hammers inakanika.
Iwo ati ndalamayi iperekedwe pasanathe masiku okwana 14.
Timuyi inagonja pa masewerowa 2-0 kuti ituluke mu chikho cha Castel Challenge ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores