"Tidzakhala ndi molalo yaikulu tikakatenga COSAFA" - Fazili
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati matupi a osewera a timuyi akuoneka kuti ndi okonzeka kugwira ntchito ndipo akukhulupilira kuti akachita bwino kwambiri ku mpikisano wa COSAFA ku South Africa.
Iye amayankhula mu tsiku lachiwiri la zokonzekera za timuyi mu m'bindikiro wawo ndipo wati ndi Sabina Thom komanso Asimenye Simwaka omwe sanafike.
Iye anati ali ndi chiyembekezo chokatenga chikho kuti adzakhale ndi molalo popita ku WAFCON.
"South Africa ndi timu ya mphamvu yomwe imatha mpira komanso tinayichinyapo nde tikayambira pomwepo. Khumbo lathu ndi lofika ndike yotsiriza ndi kutenga chikho chifukwa kutero tidzakhala ndi molalo popita ku WAFCON," iye anatero.
Iye watinso akukonza kwambiri pagolo, kumbuyo ndi pakati kuti osewera omwe amatumikira matimu a mdziko muno akhale okupsa pa mipikisanonso ikudzayi.
Malawi ili mu gulu A ndi South Africa, Angola komanso Lesotho ndipo wothera poyamba adzafika mu ndime
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores