MK Academy ipereka K1.5 million pokanika kusewera masewero
Bungwe la Football Association of Malawi lapereka chilango ku timu ya MK Academy chopereka ndalama yokwana K1.5 million kamba kosasewera masewero awo amu ligi ya amayi ya National Bank.
Timuyi inakanika kupezeka mmasewero oyenda atatu omwe amakumana ndi MDF Lioness, Ascent Academy ndi Mighty Wanderers Queens ndipo ilipira K500,000 pa masewero aliwonse.
Chilango china ndi choti anagonja 3-0 pa masewero aliwonse ndi kuwachotsera ma points zomwe zinachitika kale mkati mwa ligiyi.
Iwo auzidwanso kuti ngati sanakhutire ndi chigamulochi akamang'ale ku bungweli pasanathe maola 72.
Timuyi inakanika kuyenda kamba ka nkhani za chuma komanso kuti anali atatuluka kale mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores