Mkulu wa timu ya Master Security FC, Christopher Njeula watsimikiza kuti osewera okwana asanu ndi awiri ndi omwe timuyi yasaina padakali pano kuti atumikile mu timu yawo mu ligi ya m'dziko muno.
Osewerawa ndi monga Chikaiko Batson, Chisomo Mpachika, Precious Sambani, Anthony Mfune, Anthony Singini, Ben Manyozo komanso Goloboyi Brighton Munthali.
"Tili ndi malingaliro omanga chinthu chachikulu ku timu yathu ndipo masiku amenewa muyembekezere kuona ma bomba potengela kuti zokambirana ndi osewera ena zili mkati," anatero Njeula.
Pomaliza a Njeula ati akuchitanso zokambirana ndi team manager wakale wa Mighty Wanderers Steve Madeira kuti akhale naye limodzi potengera kuti ndi katswiri pa ntchito yake.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores