''SIZOPHWEKA KOMA TIKUNGOYENERA KUPHA BULLETS'' - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati timu yake yakonzeka kukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndi mtima woti ayigonjetse koma sizikhala zophweka poti nayonso ikufunitsitsa chipambano.
Mwansa amayankhula izi patsogolo pa masewero a matimuwa omwe aseweredwe lachitatu pa bwalo la Mzuzu ndipo wati ngati ngakhale nthawi yokonzekera ndi yochepa, osewera ali ndi njala ya masewerowa.
''Takonzeka bwino kuti tikumane ndi Bullets ndi kuti ngati zikhale bwino ndekuti tidzachite bwino. Ndikudziwa sizophweka poti anzathuwo akulimbirana ukatswiri wa ligi koma mwanjira iliyonse tikuyenera kupambana,'' iye anatero.
Timuyi ili nawo mu gulu a matimu omwe akuthawa kumunsi kwa ligiyi ndipo alinso ndi mwayi othera mu matimu asanu ndi atatu amu ligiyi ngati angachite bwino mu masewero awo.
Moyale ili pa nambala 11 ndi mapointsi okwana 33 pa masewero 26 omwe asewera mu ligiyi.
0888218915 Osward Nakoma
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores