"CASSIM ANAWAPATSA PENATE YABODZA NDIYE LERO AZIONA" - THOLE
Mlembi wamkulu watimu ya Mzuzu City Hammers, Benjamin Thole wati timuyi sinayiwalire zomwe anachita woyimbira Shaibu Cassim popereka penate yabodza kutimu ya Mighty Wanderers panthawi yomwe anakumana nayo ku Blantyre.
Iye wati pambali podzimenyera nkhondo kuti apulumuke, apanga chilichonse chothekera kuti agonjetse timuyi ngati mbali imodzi yobwezera chipongwe.
"Tikufuna kubweza chipongwe, paja pomwe timakumana nawo pabwalo la Kamuzu oyimbira Shaibu Cassim anawapatsa penote yabodza." Anatero Thole.
Pakadali pano, Mighty Wanderers ndiyachiwiri pamndandanda wa momwe matimu akuchitira muligi ya TNM ndimapointi 56 pamene Mzuzu City Hammers ili panambala 15 ndimapointi 24.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores