NYAMBOSE WAIMITSIDWA PANTCHITO KU SONGWE
Timu ya Songwe Boarder United yayamba yaimitsa pantchito mphunzitsi wake wamkulu, Christopher Nyambose kwa sabata zitatu.
Izi ndi malingana ndi kalata imene timuyi yalembera mphunzitsiyu imene yasayinidwa ndi mlembi wamkulu wa timuyi, a Palisha Swira.
Kalatayi yati ganizoli likutsatira kusachita bwino kwa timuyi pamasewero okwana 15 amene timuyi yasewera muligi ya TNM pansi pa mphunzitsiyu.
Kalatayi yaonetsanso kuti panthawi imene a Nyambose akhale asakugwira ntchito, a Edwin Kaonga ndi amene adziyitsogolera timuyi.
Pakadali pano, timu ya Songwe Border ndi yomaliza pa mndandanda wamatimu a mu supa ligi pamene ili ndi mapointi awiri okha pamasewero 19 amene yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores