FIFA YALANGA BULLETS
Bungwe loyendetsa mpira pa dziko lonse la pansi la FIFA lapereka chilango ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti isasaine osewera m'dziko muno komanso kunja mu misika yogula ndi kugulitsa osewera itatu kamba kolephera kupereka ndalama kwa katswiri wawo wa kale, Ronald Chitiyo.
Mu kalata imene Owinna yaona yati Bullets ikuyenera kulandira chilangochi kupikira atadzapereka ndalama yokwana USD15,000 yomwe ndi pafupipafupi K27.2 million.
FIFA yauzanso Football Association of Malawi kuti chibalochi chiyambe kugwira ntchito tsa'ano kuti mchitidwe womwe anachita asadzachitenso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores