Bwalo la Mulanje latsekedwa kwa sabata ziwiri
Khonsolo ya Boma la Mulanje lalengeza kuti bwalo la Mulanje Park itsekedwa kwa sabata ziwiri pomwe ikufuna kukonzanso zinthu zingapo zomwe zaonongeka pa bwaloli.
Mu kalata yosainidwa ndi wong'anira gawo la zamasewero ku khonsoloyi a Sherif Malunga kupita ku Komiti yoyendetsa mpira ku Mulanje yati bwaloli likhala lotseka kuchokera pa 11 September mpaka pa 25 September 2025.
Iwo ati pa nthawiyi akhale akuthilira kapinga komanso kutchetcha mwa dongosolo cholinga choti posewerera pakhale pabwino.
Iwo atinso alembera mabungwe a Football Association of Malawi, Southern Region Football Association komanso timu ya FOMO za uthengawu.
Timu ya FOMO ndi imene imagwiritsa kwambiri bwaloli mu masewero awo amu NBS Bank National Division League komanso timu yawo yachisodzera mu Thumbs Up Southern Region Football League ndipo kumathero a sabatayi FAM inayika masewero a timuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores