"Ndi nthawi tsopano yobwenzera nkhonya kwa Civil" - Kananji
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji, wati tsopano timu yake ikuoneka kuti ilibwino pomwe anyamata ayamba kuzolowera zomwe amawaphunzitsa ndipo akapeza chipambano pomwe akuyamba Chigawo chachiwiri cha Supa ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Civil Service United loweruka pa bwalo la Aubrey Dimba ndipo wati abwenzera chipongwe kamba koti anagonja 2-0 mchigawo choyamba.
"Akhala masewero ovuta pakuti anatigonjetsa mchigawo choyamba chija Koma apa tikufuna tikabwenzere nkhonya ndipo anyamata ali okonzeka kukachita bwino poti zomwe ndikumawaphunzitsa ayamba kuzimva nde tiyembekezere zabwino." Anatero Kananji.
Iye wati wayang'ana kwambiri nkhani yomwetsa zigoli pomwe timuyi ikuoneka kuti ikumavutika ndipo watsimikiza kuti akapeza zochuluka ndi Civil.
Timuyi ili pa nambala 11 mu ligi ndi ma points okwana 18 poti inapambana kasanu kufanana mphamvu katatu ndi kugonja kasanu ndi kawiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores