"Hammers situluka mu ligi" - Chirambo
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Elias Chirambo, wati ndi okondwa kuti timu yake tsopano ikugwirana ndipo wauza ochemelera atimuyi kuti siyituluka mu ligi.
Iye amayankhulapo kutsatira kusachita bwino kwa timuyi pomwe ili pa nambala 15 kusemphana ndi momwe imachitira chaka chatha pomwe inathera pa nambala yachinayi.
Koma Chirambo wati tsopano timuyi ikupereka chilimbikitso ndi mmene inasewera ndi Creck Sporting Club ngakhale anagonja 1-0 ndipo iwo azitolera.
"Panopa tsopano zikuoneka kuti timu yagwirana ndekuti mmasewero akudzawa tikhale tikuchita bwino. Hammers sikutuluka mu ligi chaka chino." Anafotokoza Chirambo.
Timuyi yatsala ndi masewero anayi mchigawo choyamba pomwe ikumane ndi Mighty Wanderers, Silver Strikers, FCB Nyasa Big Bullets komanso Civil Service United.
Timuyi ili ndi mapointsi asanu ndi atatu pomwe yapambana kawiri, kulepherana kawiri ndi kugonja kasanu ndi kawiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores