"Tayitaya tokha ya lero" - Ngwira
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Alex Ngwira, wati timu yake yakanika kupeza chipambano pamwamba pa timu ya Ekhaya FC osati kuti masewero anali ovuta Koma kuti aphonya okha mipata yabwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anathera 0-0 pa bwalo la Dedza ndipo anati timu yake inasewera mwapamwamba poti Ekhaya yakhalira kumaka.
"Anali masewero osati ovuta Koma tachitaya tokha chifukwa anyamata a Ekhaya akhalira kumaka Koma kuti mpata yabwino yomwe tinapeza takanika kugwiritsa ntchito." Anatero Ngwira.
Iye anati timuyi tsopano ilibwino Koma akufunikira wosewera m'modzi wa kutsogolo kuti awathandize kuti mipata yomwe akumapeza azitha kugoletsa.
Timuyi ili pa nambala 7 ndi mapointsi okwana 14 mu masewero 11 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores