Dedza yakonzeka kukumana ndi Wanderers
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Alex Ngwira, wati timu yake sinakonzekerenso mosiyana ndi momwe amakonzekerera mmasewero onse ndipo akukhulupilira kuti achita bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mighty Wanderers pa bwalo la Kamuzu lamulungu ndipo wati timu yake yaika mulingo woti azisewerera kuti akagwirana asamavutike koma akonzeka kwambiri.
"Timu yonse ilibwino ndipo palibe osewera yemwe ali ovulalala. Takonzekera monga momwe timakonzekerera palibenso kuti tikukumana ndi timu ina yaikulu kuposa inzake poti matimu onse ndi ovuta komabe takonzekera bwino." Anatero Ngwira.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri pomwe ili ndi mapointsi okwana 13 pa masewero 9 omwe yasewera mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores