"Tidzukira pa Moyale ndithu" - Nyoni
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, watumiza uthenga wokoma kwa otsatira timuyi kuti ayesetsa kugwiragwira monse momwe amavutika ndipo timuyi iyamba kuwamvetsa kukoma posachedwa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a timuyi ndi Moyale Barracks pa bwalo la Rumphi ndipo wati iyi yokha apha ndi nyundo zawo poti agonja kwambiri mu ligiyi.
"Ndi masewero ovuta kwambiri koma tagonja mowilikiza nde tayesetsa takonza ndipo masewero awa nde podzukira pathu ndipo omwe amasapota timuyi ayamba kumva kukoma." Anatero Nyoni.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi ma points okwana anayi pa masewero 6 omwe yasewera poti yapambana kamodzi, kufanana mphamvu kamodzi ndi kugonja kanayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores