"Ndimangomva kuti ku Karonga kuli Oyimbira" - Makonyola
Mphunzitsi wa timu ya Mitundu Baptist, Audrow Makonyola, wati Oyimbira aku Karonga amachita kukonza kuti timu ina yobwera isachite bwino ndipo poyamba ankangomva koma tsopano apa watsimikiza atapitako.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anagonja 1-0 ndi timu ya Baka City kukhala kugona koyamba mu ligi ya NBS National Division League ndipo wati timu yake inali bwino koma oyimbira anayida.
"Tinangomva kuti ku Karonga kuli Oyimbira omwe amachita kukhala ngati amapatsidwa masewero kuti timu ina iluze, Red Lions inadandaulako koma apa taziona. Ngati zipitilire Izi ndekuti sitikhala ndi mpira wabwino mu ligiyi." Anatero Makonyola.
Iye watinso timu yake ili ndi mkwiyo waukulu kamba kogonja mmasewerowa ndipo timu idzazisiya akayipeza kwawo.
Timuyi ikadali pamwamba pa ligi ndi mapointsi asanu ndi anayi pa masewero anayi mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores