TUNISIA YAIPONYERA KWAKUYA
Timu ya dziko la Tunisia yatsegula mpata wa mapointsi asanu pamwamba pa gulu H momwe mulinso dziko la Malawi kutsatira kukwapula timu ya Liberia 0-1 lero madzulowa.
Chigoli cha katswiri wotchedwa Hazem Mastouri chobwera pa mphindi zinayi za masewerowa chinali chokwanira kuti timuyi idye monona mwa timu ya Mario Marinicayi.
Zateremu Tunisia ili pa nambala yoyamba ndi mapointsi 13 pomwe Namibia ili pachiwiri ndi mapointsi asanu ndi atatu (8) ndipo pachitatu pali Liberia ndi mapointsi asanu ndi awiri (7).
Malawi ili ndi asanu ndi Imodzi (6), Equatorial Guinea atatu komanso Sao Tome and Principe ilibe point iliyonse pa matimu omwe ali kumunsi mu gululi.
Koma timu ya Malawi ili ndi mwayi wofika pa nambala yachiwiri ngati igonjetse Namibia mawa kenako masewero otsatira ndi kukakumana ndi Tunisiayo pa 24 March 2025.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores