TNM sikuonjezera ndalama
Kampani imene imathandiza ligi yaikulu mdziko muno ya TNM Plc yati sikuonjezeanso ndalama zomwe akupereka ku TNM Supa ligi ndipo ndalama zikhalebe K500 million pa chaka.
Mkuluyi woyang'ana za malonda ku kampaniyi, Sobhuza Ngwenya, ndi yemwe wayankhula izi pa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe pomwe wayankhula za mwambo wopereka mphoto womwe uliko lachisanu likudzali.
Iye anati: "Tikudziwa kuti moyo wadula padakali pano koma tinakweza ndalama chaka chija nde apa tikukhulupilirabe kuti sikuti zikadali poyipa ndithu."
Mgwirizano wa ndalamazi womwe anasainirana ndi Super League of Malawi utha chaka cha mawa.
Ligi ya chaka chino ikuyamba pa 05 April 2025 ndi masewero otsegulira kukakhalapo pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe pomwe Silver Strikers idzalandira FCB Nyasa Big Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores