"TACHOKERA KUTALI" - IKWANGA
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Kondwa Ikwanga, wati timu yake yakonzeka bwino kwambiri kuti ichite bwino ndipo masewerowa si achilendo poti achokera kutali.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero amu ndime yotsiriza mu chikho cha Castel Challenge masana a loweruka pa bwalo la Bingu pomwe akumane ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers.
Iye wati akonzeka bwino kuti achite bwino ndipo kutali komwe achoka osati kuyenda koma mu mpikisanowu.
"Tinayamba kukonzekera masewerowa kalekale nde anthu ayembekezere mpira wabwino kwambiri pa Bingu." Anatero Ikwanga.
Timuyi inagonjetsa FCB Nyasa Big Bullets 4-1 mu mapenate mu mphindi 90 masewero atatha 0-0 kuti afike mu ndime yotsiriza ndipo ndi Wanderers akumana kawiri pomwe anapambana 2-0 mchigawo choyamba asanagonje 8-0 mchigawo chachiwiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores