"ATOLANKHANI MUMAKOKOMEZA, PALIBE CHASINTHA" - MPONDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Flames, Peter Mponda, wati kupambana kwa timu ya Malawi kusachotse ulemu wa mphunzitsi yemwe wachoka kutimuyi, Patrick Mabedi, poti iye ndi Kalisto Pasuwa palibe chimene asinthako ku timuyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe Malawi yapambadza Burkina Faso 3-0 pa bwalo la Bingu ndipo wati anthu asayankhule kwambiri poti asewera bwino ndi osewera osati aphunzitsi.
"Penapake atolankhani mumasokoneza zinthu nde ndikuuzeni palibe chimene chasinthako kutimuyi ndipo tisachotse ulemu kwa mphunzitsi yemwe analipo nde pena kukabwera aphunzitsi atsopano choncho amalimbikira akakhazikika amatayilira." Anatero Mponda.
Iye watinso ntchito yomwe anatumidwa agwira ndipo sakudziwa chilichonse chokhudza tsogolo lawo ndipo wati aphunzitsi omwe abwere kutimuyi adzakhalanso ndi ntchito yawo pomwe yawo yatheka.
Malawi tsopano yamaliza pa nambala yachitatu mu gulu lawo pomwe yatolera mapointsi anayi omwe apezeka
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores